MUUNI WA ZA LUSO LA MAKONO NDI DANIEL BANDA
Tsopano timve za Muuni wa za luso la makono ndi Daniel Banda, ndipo lero akusimba za makono a makina osakaniza chakudya cha nkhuku.
BUNGWE LA UNITED PURPOSE KU MOZAMBIQUE LIKHAZIKITSA MALO OTUNGIRA MADZI A UKHONDO
Bungwe la United Purpose mu dziko la Mozambique, likufuna kukhazikitsa ntchito yopereka madzi a ukhondo ochokera mu mpope m’ma midzi. Bungweli, lati projectiyi ndi ya ndalama zokwana $10milion, ndipo alimi athandizika pa nkhani yosowa madzi. Mtolankhani wathu Bright Sonjera wadza ndi nkhaniyi.
NJOBVU ZAYAMBA KUSAMUTSIDWA KUCHOKA KU LIWONDE NATIONAL PARK KU MALAWI
Boma la Malawi layamba ntchito yosamutsa njobvu zokwana 250 komanso nyama zina ndi zina kuchokera ku Liwonde National Park kupita ku Kasungu National Park, komwe ndi malire ndi dziko la Zambia. Mtolankhani wathu George Mhango walankhula ndi Bright Kumchedwa yemwe mkulu wa bungwe loyang’anira mal…
ANTHU ASANU AGAMULIDWA KUTI AKHALE MDENDE MOYO WAWO ONSE KU MALAWI
Anthu ambiri alankhulapo pa gamulo lomwe bwalo la milandu mdziko la Malawi, lagamula kuti anthu asanu omwe anapha mwa nkhanza munthu wa chi albino, Mc Donald Masambuka mu chaka cha 2018 akhale m’nende moyo wawo onse. Mtolankhani wathu Jane Chilimampunga wadza ndi nkhaniyi.
MTSOGOLERI WA DZIKO LA ZAMBIA WATI MAFUMU AKUYENERA KUKWEZA NAWO CHITUKUKO
Anthu mu dziko la Zambia apelenga ndemanga pa mawu omwe mtsogoleri wadzikolo Hakainde Hichilema, walankhula kuti nzika za dzikolo komanso mafumu, atenge nawo gawo pa mbali yokweza chitukuko cha dzikolo. Mtolankhani wathu Ziyenela Zimba walankhula ndi Headman Kalinde wa m’chigawo cha ku m’mawa kwa d…
MOZAMBIQUE AKUKUMBUKUKILA TSIKU LOMWE ANAKHALA OYIMA PAYEKHA
CHINYANJA: Lero pa 25 dziko la Mozambique likukumbukila tsiku lomwe linakhala dziko loyima palokha ndipo linachoka mmanja mwa atsamunda. Dzikoli lakwanitsa zaka 47 chitengeleni ufulu.
MKULU WA POLISI KU MALAWI GEORGE KAINJA WATULUTSIDWA PA BELO
CHINYANJA: Amene anali ndi mkulu wa polisi mdziko la Malawi a George Kainja atulutsidwa pa belo lero pambuyo pomangidwa dzulo pa mlandu olowelela pa kafuku fuku wa katangale yemwe mpondamatiki Zuneth Sattar anachita.
NKULU WA BUNGWE LA BUTEZ KU ZAMBIA WATI BOMA LILEMBE NTCHITO NZIKA ZA ZAKA 45
Nkulu wa bungwe la aziphunzitsi la Basic Education Teachers Union of Zambia kuchigawo cha kummawa Simon Botha wati chingakhale chinthu chobweretsa nsangala ngati boma lingalembe ntchito aphunzitsi a zaka zokwana 45 zakubadwa kapena kupyola pangono, Malamulo a dziko la Zambia amaletsa boma kulemba a…
NDEMANGA YA KATSWIRI PA ZA MALAMULO KU MALAWI PA NKHANI YA CHILIMA NDI CHAKWERA
Katswiri pa malamulo a dziko la Malawi garton Kanchedzera wathilira ndemanga potsatira mau a mtsogoleri wa dzikolo Lazarus Chakwera oyimitsa ntchito za wachiwiri wake Saulos Chilima yemwe pamodzi ndi anthu ena akukhudzikdwa ndi katangale ndi ziphuphu malingana ndi lipoti la bugwe lakafukufuku la AC…
PALI KUFUNIKA KUPHUNZITSA ANTHU PA NKHANI YA MATENDA OPATSIRANA POGONANA KU MALAWI
M’modzi mwa akatswiri a za umoyo pa matenda opatsira pogonana mu dziko la Malawi, George Jobe walankhula pa kufunika kuphunzitsa anthu pa chiopyezo kwa kugonana kosadziteteza. Mtolankhani wathu Hastings Blessings Jumbe akusimba.