

Boma la Zambia lasayina pangano la za umoyo ndi boma la USA la $2.49 biliyoni
Boma la Zambia lasayina pangano la za umoyo ndi boma la United States of America la ndalama zokwana 2.49 biliyoni US dollars ndipo unduna wa za umoyo wati ndalamazi zithandizila kupititsa patsogolo ntchito za umoyo mdziko la Zambia. Ziyenela Zimba akutambasula bwino nkhaniyi

Vuto la kusowa kwa mafuta agalimoto likupitilira ku Malawi
Anthu ambiri mdziko la Malawi adzudzula bungwe lowona za mafuta ndi magetsi la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) ndi bungwe lokhometsa msonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) polekelera ma venda kumagulitsa mafuta agalimoto pa msika osavomelezeka komanso okwera mtengo kwambiri pamene ma…

Madera ambiri a dziko la Zambia akuyembekezeka kulandira mvula yochepa kwambiri
Madera ambiri a dziko la Zambia akuyembekezeka kulandira mvula yochepa kwambiri komanso zokolola zochepa m’nyengo ya ulimi ya 2026/2027. Ichi ndi chifukwa cha nyengo ya El Nino yomwe idzakhudza madera ambiri adzikolo. Izi zapangitsa akatswiri azanyengo komanso unduna wa za ulimi kupempha alimi kuti…

Boma la Zimbabwe liyendetsa maliro a mponda matiki Wicknell Chivayo
Boma la Zimbabwe ndi lomwe liyendetse maliro a mponda matiki Wicknell Chivayo ndi mkazi wake Lucy Muteke amene anamwalira pa ngozi ya helicopter ndi anthu ena atatu sabata yatha. John Kassim akufotokoza mwatsatane-tsatane.

Brian Mundubile ndi Makebi Zulu a Tonse Alliance ku Zambia awonekela ku khothi
Mtsogoleri wa mgwilizano osutsa boma wa Tonse Alliance Pamodzi mdziko la Zambia Brian Mundubile ndi wachiwiri wake Makebi Zulu lero anawonekela ku bwalo la milandu m’boma la Solowezi ndipo khothi lakana pempho la akulu akuluwa lofuna kupeleka umboni wa pakamwa pa mlandu omwe akuzengedwa ochita zok…

Lefutenanti Mabonga watulutsa kanema owonetsa anthu ena akuzunzidwa ku Uganda
Msilikali wina wadziko la Uganda Lefutenanti Matanda Mabonga watulutsa makanema omwe akuonetsa anthu ena omwe amazuzidwa akagwidwa kunyumba zomwe asilikali adzikolo a UPDF anamanga pofuna kulangiramo anthu otsutsa boma zija pachingerezi amati ma safe house kapena torture chambers.Mtolankhani mzathu…

Matenda a Cholera ayamba mu mzinda wa Lusaka ku Zambia
Bungwe loyang’anila za umoyo pa dziko lonse la pansi la WHO, lapempha adindo a boma la Zambia kuti alimbike pa ntchito yothana ndi matenda a Cholera omwe abuka kale mu mzinda wa Lusaka likulu la dzikolo. Ziyenela Zimba ali ndi nkhani yonse.

Bungwe la ACB ku Malawi lamanga mkulu wakale wa asilikali Gen Valentino Phiri
Bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu mdziko la Malawi la Anti Corruption Bureau - ACB, lamanga mkulu wakale wa asilikali a nkhondo General Paul Valentino Phiri pomuganizira pa milandu isanu yokhudza kugwiritsa ntchito udindo wake molakwika komanso kugwiritsa ntchito katundu opezeka mu njira zo…

Prezidenti waZimbabwe Emmerson Mnangagwa wapepesa zaimfa yaChivayo ndi ena asanu
Prezidenti wa dziko la Zimbabwe Emmerson Mnangagwa wapeleka uthenga wa chipepeso kwa Mabanja a Mpondamatiki odziwika bwino wa mdzikolo Wicknell Chivayo yemwe wamwalira pangozi ya helikopita pamodzi ndi mkazi wake Lucy Muteke ndi anthu ena anayi. John Kassim akulongosola zambiri.

Mtsogoleri wa dziko la Mozambique Daniel Chapo akucheza mdziko la Botswana
Mtsogoleri wa dziko la Mozambique Daniel Chapo akucheza mdziko la Botswana komwe akumane ndi mtsogoleri wa dzikolo Duma Boko ndi kulimbikitsa ubale pakati pa mayikowa pa ntchito zosiyana siyana monga ulimi ndi maphunziro. Bright sonjela akulongosola nkhani yonse mwatsatane tsatane.