



Anthu ena ku Malawi akufuna nthambi zina za boma zikhale zoyima pa zokha
Anthu ena mdziko la Malawi akufuna kuti mabungwe ndi nthambi zina za boma zikhale zoyima pa zokha kuti boma lisamalowelere pa kagwilidwe ka ntchito zawo pamene ena akufuna kuti bungwe loyendetsa chisankho la MEC likhale loyima pa lokha. Jayne Chilimampunga wabwela ndi nkhani yonse

Boma la Mozambique lakhwimitsa chitetezo cha mankhwala ndi makatemela
Boma la Mozambique lakhwimitsa chitetezo cha mankhwala ndi makatemela ochokela kunja. Bright Sonjela akulongosola zonse

Linda Kasonde, Brebner Changala apeleka chikalata chotsutsa masankho a ku Zambia
Loya komanso womenyera ufulu wa anthu, a Linda Kasonde, a Brebner Changala ndi bungwe la LCK Freedom Foundation, apereka petition kapeni kuti chikalata ku Constitutional Court mdziko la Zambia, kupempha khotili kuti lilamule kuti pakhale chisankho china cha President, ponena kuti chisankho cha pa 1…

Akatswili pa nkhani ku Malawi akhumudwa ndi kubedwa kwa K700 miliyoni ku NOCMA
Akatswiri omwe amayankhulapo zochitika zosiyana-siyana mdziko la Malawi, ati mzovetsa chisoni kuti adindo alephera kuteteza ndalama zomwe zabedwa ku company yowona za mafuta agalimoto ya NOCMA zokwana K700 million. Kondwani Nyamasauka ali ndi nkhani yonse.

Akatswiri a zamalamulo ku Uganda atsutsa zakutula pansi kwa maloya aKizza Besgye
Akatswiri a za malamulo ambiri ku Uganda atsutsana ndi zomwe zachitika ku bwalo lamilandu la likulu ku Uganda pomwe maloya oyimira mulandu nkhalakale pandale a Kizza Besigye ndi anzawo a Obed Lutale anena kuti asiya kuwayimira iwowa pa mulandu wawo.Awiriwa akuyankha mulandu ofuna kulanda boma ladzi…

Makhothi onse atsekedwa mdziko la Zambia
Makhothi onse m’dziko la Zambia atsekedwa ndipo akuyang’aniridwa ndi asilikali, pomwe lero pa 24 August 2026 ndi tsiku lomaliza loti mtsogoleri wa Tonse Pamodzi Alliance, Brian Mundubile, apereke patition kapena kalata yotsutsa zotsatira za chisankho cha pa 13 August 2026. Zimenezi zachititsa kuti…

Anamwino 500 a mdziko la Malawi azapita ku Israel kukagwila ntchito
Ntchito yothandiza anamwino 500 a mdziko la Malawi kuti akagwile ntchito ku Israel chaka chino, yafika ku mapeto pamene mazana mazana anamwino omwe analamaliza maphunzilo awo sakugwila ntchito Ku Malawi. George Mhango wabwela ndi nkhani yonse

Mzika za Zambia zomwe zili ku South Africa zikufuna boma la UPND likonze zinthu
Mzika zina za dziko la Zambia zomwe zikukhala mdziko la South Africa zati masankho omwe anachitika sabata yatha mdzikolo akukhudza tsogolo la mabanja awo, chuma cha dziko, komanso chiyembekezo cha moyo wabwino. Channel Africa yacheza ndi zina mwa nzikazi mu mzinda wa Johannesburg mdziko la South A…

Nambala ya omwalira pa ngozi ya boti pa Nyanja ya Kariba ku Zimbabwe ili pa 92
Apolisi ndi asilikali akupitilira kufufuza anthu amene anasowa pangozi ya boti pa Nyanja ya Kariba mdziko la Zimbabwe lachiwiri sabata yatha pamene chiwelengelo cha anthu omwalira chafika pa 92. John Kassim akulongosola zonse.

Mtsogoleri wa Zambia Hakainde Hichilema wapambana masankho
Pulezidenti Hakainde Hichilema wayamikira anthu onse a ku Zambia, kuphatikizapo amene anamuvotera komanso amene sanamuvotere, potsindika kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha mtsogoleri amene akumufuna.Malinga ndi zotsatira za masankho zomwe zalengezedwa ndi bungwe loyendetsa zisankho la ECZ,a Hich…