Anthu ambiri akufuna kuti boma likhazikitse lamulo loti opha nzake naye aziphedwa, ndikuti president azisainira.Izi zadza pamene mchitidwe ophana chisawawa ukunka nuchulukira ku Malawi. Sabata yatha ku Mwanza anthu anapeza mafupa a ana aakazi awiri wina zaka 10 wina 12 mminda yosiyana, atasowa kwa masiku ambiri. Jayne Chilimampunga wadza ndi nkhaniyi

Mary Chilima wayamikila Mutharika mtsogoleri wa Malawi pofufuza imfa ya Chilima
08:31

Kachilombo ka Polio 2 kapezeka mu mzinda wa Lusaka ku Zambia
05:48

Mtsogoleri wa Zambia Hakainde Hichilema wachotsa nduna ziwiri
08:43