Anthu pafupifupi 300 amene akukhudzidwa ndi kuphedwa mwa nkhanza kwa mai wa ntchito za malonda, Hellen Kamutumbe , amangidwa ndi A polisi mu boma la Kalumbila ku chigao cha North-western Province cha dziko la Zambia. Maiyu anavulidwa ndi kugendedwa miyala ndi anthu okwiya Lachisanu lathali pamene mnyamata wa zaka 25 zakubadwa ananamizila maiyu kuti anamubela maliseche ake mwa matsenga pa msika wa Kisasa mu bomali. Daniel Elisha Banda akulongosola.

Mafuta agalimoto akwera ku Malawi ndi 35%
06:44

Apolisi ku Kenya amanga nduna yakale chifukwa chonamizila kubedwa
06:05

Nyumba ya malamulo ku Malawi yakhazikitsa komiti yofufuza imfa ya a Chilima
08:07