Zipani za mgwirizano zotsutsa boma za mdziko la Zambia za Tonse Alliance zapambana chisankho cha phungu ku dera la Chawama mu mzinda wa Lusaka. Masankhowa achitika dzulo pambuyo pa yemwe kale anali phungu wa deralo, Tasila Lungu, kuchotsedwa pa mpando ndi nyumba ya malamulo . Ichi ndi chifukwa chakuti maiyu adakhalitsa miyezi yochuluka kopanda kuonekera mu nyumba ya malamulo kamba kakuti amalira maliro abambo wake Edgar Chagwa Lungu yemwe kale anali mtsogoleri wa dzikola Zambia. Nkhani yonse ili ndi Daniel Elisha Banda.

Anthu a chi alubino akupitilira kuchitidwa nkhanza ku Malawi
07:17

Alimi ena ku Zambia akudikilabe boma liwapatse malipiro atagulitsa mbewu ku FRA
07:55

Akatswili a ndale ati A Mutharika akutsogolera bwino Malawi
06:24