Purezidenti wa dziko la South Sudan, Salva Kiir, wachotsa ntchito Spikala wa Nyumba ya Malamulo komanso wachiwiri wake. Muchidziwitso chomwe chalengezedwa m’Nyumba ya Malamulo Lachiwiri ndi Tulio Odongi Ayahu, yemwe ndi mkulu wa chipani cholamula cha SPLM ,chati amene achotsedwa ndi Jemma Nunu Kumba, omwe anali Spikala ndi wachiwiri wake Permena Awerial Aluong.Izi zikubwera pambuyo poti mamembala a chipani cha SPLM apereka madandaulo akuti Kumba anali ndi mlandu wa ziphuphu zokhudzana ndi kugwiritsa ntchito molakwika ndalama za Nyumba ya Malamulo. Alfred Dzaoneni wadza ndizambiri.

Mabungwe ena ku Malawi adzudzula zomwe Alexious Kamangila akulankhula
07:45

A katswili andale ena ku Malawi ati a Chakwera sanalankhule bwino pa maliro
06:45

Mchitidwe wa anthu otengela lamulo m’manja wakula ku Zambia
06:26