



Bungwe la MANEB ku Malawi latulutsa zotsatila za mayeso a standadi 8 ndi fomu 2
Bungwe lowona za mayeso mdziko la Malawi la Maneb latulutsa zotsatila za mayeso a standadi 8 ndi fomu 2. Jayne Chilimampunga wabwela ndi nkhaniyi ..

Polisi ya Zambia yagwira akuluakulu 11 azipani zotsutsa za mgwirizano wa Tonse
Polisi ya dziko la Zambia yagwira akuluakulu khumi ndi m’modzi 11 azipani zotsutsa za mgwirizano wa Tonse Alliance pambuyo pakupezeka ndi zida za nkhondo zoopsya. Mkulu wa zipanizi ndi a Brian Mundubile amene akutengako mbali ku masankho a President. Pakati pa wogwidwawa pali mpongozi wa malemu E…

Mabungwe ku Zimbabwe adzudzula boma kuti likuwononga ufulu opanga zionetselo
Mabungwe omenyela ufulu anthu mdziko la Zimbabwe, adandaula kuti boma likuphwanya ma ufulu a anthu pamene anthu ena anamangidwa lachisanu sabata yatha chifukwa chofuna kuchita zionetselo. John Kassim akulongosola zonse..

Mtsogoleri wa Zambia Hakainde Hichilema wadzudzula ziwawa pa ndale
Mtsogoleri wa dziko la Zambia Hakainde Hichilema, wadzudzula ziwawa za ndale zomwe zikuchitika m'madela ena a mdzikolo komanso salora kuti anthu azinzuzidwa ndi kuchitidwa nkhanza chifukwa cha ndale ndipo yemwe apezeke akutelo, lamulo lizigwila ntchito pa iye. Ziyenela Zimba wadza ndi zambiri...

Amayi akulimbikitsidwa kuti aziyamwitsa makanda mkaka wa m’mabele
Dziko la Malawi likukumbukila nawo sabata yolimbikitsa amayi kuyamwitsa ana komanso mwa kathithi ndi cholinga chokuti ana azikula mwa thanzi pamene mayiko pa dziko lonse la pansi akukumbukila sabatayi. Jayne Chilimampunga ali ndi zambiri za nkhaniy...

A Suleman apempha kuti madraiva oledzela azigula ma polo omwe awononga ku Malawi
Pamene ngozi komanso kuonongeka kwa katundu wa mu misewu ikulu ikulu kwafika poonjeza mdziko la Malawi, spikala wa nyumba yamalamulo mdzikolo wapempha aphungu kuti akhazikitse lamulo lokhwimitsa zilango kwa anthu omwe amayendetsa galimoto ataledzera ndi kugwetsa mapolo amagetsi amunsewo azikonza o…

Mozambique,Tanzania ndi Malawi, akhazikitsa nthambi ya Rovuma River Basin
Mayiko a Mozambique, Tanzania ndi Malawi, amaliza ntchito yokhazikitsa nthambi ya Rovuma River Basin yomwe iziyendetsa ndondomeko zakagwilitsidwe ntchito ka mitsinje ndi nyanja zomwe mayikowa amagawana. Bright Sonjela ali ndi nkhani yonse

A Sylvester Namiwa awatchaja mlandu wa kulanda boma mwa upandu ku Malawi
Mkulu wa bungwe la CDEDI mdziko la Malawi a Sylvester Namiwa awapatsa milandu iwiri , yofuna kulanda boma mwa upandu ndi kugawa uthenga wabodza. A Namiwa pakali pano akusungidwa ku ndende ya Maula pamene akuyembekezela kuti apatsidwe belo. George Mhango wabwela ndi nkhaniyi

Zimbabwe yatsutsa kuti chakudya chikuchepa kwa anthu omwe anathawa kuSouthAfrica
Boma la Zimbabwe lakana nkhani yokuti chakudya chikupelewela kwa anthu amene ali ku Bulawayo omwe achoka ku South Africa pambuyo powukilidwa chifukwa chokhala mdzikolo mosavomelezeka . John Kassim akusimba...

Mzika 51 za ku Mozambique zawotcheledwa nyumba ku South Africa
Anthu okwana 51 a mdziko la Mozambique amene akukhala ku South Africa akusowa pokhala pamene nyumba zawo pomodzi ndi katundu zaotchedwa m’dela la Mamelodi mu mzinda wa Pretoria. Bright Sonjela akufotokoza nkhani yonse.