Khothi mdziko la Uganda lalamula boma la dzikolo kuti lipeleke ndalama zokwana 10 miliyoni za Ugandan shillings ($2,740) kwa aliyense amene anazunzidwa ndi Thomas Kwoyelo, mkulu wa gulu la zigawenga la Lord's Resistance Army, yemwe ndi munthu woyamba wamkulu mu gulu limeneli kupezeka ndi mlandu ndi khothi la ku Uganda pamene gululi linapezedwa kuti linapha ndi kugwilira anthu komanso kuchita anthu ukapolo ku mpoto kwa dzikolo mu zaka za ku mbuyoku. Alfred Dzaoneni akufotokoza zambiri.