Boma la Zimbabwe likufuna kukhazikitsa lamulo lokuti munthu opezeka ndi mlandu ogwilira azilembedwa mu buku la akaidi opalamula milandu yochita nkhanza kwa amayi ndi ana pamene dzikolo likukumbukila masiku 16 othandiza kuchepetsa nkhanza kwa amayi ndi atsikana.
John Kassim akulongosola nkhaniyi.