Presidenti wa dziko la South Africa, Cyril Ramaphosa, wati posachedwapa pakhala mkumano ofuna kukambirana nkhani yokhudza nkhondo yomwe ikuchitika mchigawo cha North Kivu mdziko la Democratic Republic of Congo.
Izi, ndi mwa zina zomwe Ramaphosa walankhula m’mawa wa lero pa mkumano ndi presidenti wa dziko la Angola, Joao Lourenco, yemwe alipa ulendo wa tsiku limodzi ku dzikoli.
Mkumanowu, unachitikira pa ma ofesi a boma otchedwa Union Buildings mu mzinda wa Pretoria.
Thamo Kapisa anali nawo ku nkumanowu ndipo wabwela ndi ripoti ili.