Mamembala ena a UPND kuZambia akufuna nthawi ya Prezidenti yolamula ayiwonjezeleAtsogoleri ena a chipani cholamula boma cha UPND ku Zambia akufuna kuti Nyumba ya Malamulo ichotse malire a nthawi ya utsogoleri wa Prezidenti, omwe malinga ndi malamulo a dzikolo ndi zaka khumi. Malinga ndi malamulo omwe alipo, Purezidenti Hakainde Hichilema akuyenera kumaliza nthawi yake yachiwiri mu chaka cha 2031. Komabe, ngati kusintha kwa lamuloli kungavomerezedwe, Purezidenti Hichilema angakhale ndi mwayi wopikisana pa chisankho china, malinga ngati adzasankhidwenso ndi anthu. Daniel Elisha Banda akulongosola.